Artist: Newstar Malawi
Song title: Real Love
(Verse 1)
Panali tsikana, ndinkamufuna,
Koma kumuza, zakukhosi kwanga,
Sankalabadira, anapitilizabe,
Kufikira tsiku, lowawa kwambiri moyo wanga.
(Chorus)
Anali ndimamuna wina, oneka ochokera kochita bwino,
Anandinyoza, pamaso pa iye,
Ndinachita manyazi, zinandiwawa,
Koma ndinamvomereza, zikundiwawa muntima.
(Verse 2)
Pakupita panthawi,
Ndinapeza nkazi,
Yemwe ankandikonda,
Posatengera maonekedwe kapena chilichonse chaine.
(Chorus)
Tinauyamba ulendo, wathu wachikondi,
Tinatenga maloto ngati njira yathu, ndikuwakwanilitsa,
Pamapeto pake, nkazi ankandikana uja, anabwera kwaine akulira.
(Bridge)
Anabwera pamaso panga,
Napempha kuti, tibwereraneso,
Koma mtima wanga unakana.
Tinauyamba ulendo, wathu wachikondi,
Tinatenga maloto ngati njira yathu, ndikuwakwanilitsa,
Pamapeto pake, nkazi ankandikana uja, anabwera kwaine akulira.
Anabwera pamaso panga,
Napempha kuti, tibwereraneso,
Koma mtima wanga unakana.
(Outro)
Chikondi cheni cheni, chimakhalitsa, sichimaona maonekedwe.
Okukonda zeni zeni ngakhale muzowawa, samakusiya,
Nkhani yachikondi, imapitilira,
Akondeni okondedwa anu nthawi zonse.