Intro....
Ahh.... ahh.... mmhh,
Ohh.... ohh.... mmhh,
It's Newstar Malawi
Nyimbo zachikondi
Zoti umandikonda ndimadziwa,
Zoti ndimakukonda umadziwa,
Ndikufuna undilonjeze,
Ukuyenera kunena mochokera pansi pa ntima.
Ukuti wakonzeka kulowa nane m'banja,
Ndikufuna undilonjeze,
M'banja timakumana ndi zambiri,
Pali nyengo zambiri zowawa,
Pena timatha kugona ndinjara,
Pena kudya ndiwo zopanda mafuta.
Ukuyenera kukandikonda ndi ntima onse,
Ukuyenera kundilonjeza kuti sunzandisiya,
Ngakhale tidzakumane ndinyengo zowawa,
Ndawuzidwa zambiri ati ubare wathu sungatheke.
Ena akumati sitimakhalana,
Ena mpaka kumanena kuti sitidzasamalana,
Ndangowauza kuti zatsogoro lathu akudziwa ndi mulungu,
Ndakakamira chifukwa ndimakukonda.
Tikamvana chimodzi, tidzakhala ndi mphamvu, tidzathana ndi nyengo zonse zowawa.
Ngakhale tingakumane zowawa, tisakayike, tilimbe ntima,
Chida chachikulu, ndikukondana.
Zoti umandikonda ndimadziwa,
Zoti ndimakukonda umadziwa,
Ndikufuna undilonjeze,
Ukuyenera kunena mochokera pansi pa ntima.
Ukuti wakonzeka kulowa nane m'banja,
Ndikufuna undilonjeze,
M'banja timakumana ndi zambiri,
Pali nyengo zambiri zowawa,
Pena timatha kugona ndinjara,
Pena kudya ndiwo zopanda mafuta.
Undilonjeze kuti sudzasintha mawanga, ndikundisweranso ntimawanga.