[Intro]
Aaayeeee it's George Chigome!!! again
[Verse]
Gir Ndidakukonda poyamba pompaja, ndidakuponyela mau iwe sumkayankha, ndinayesa kulimbika iwe unakana, poyankha pako umkati si type yanga, unatengeka ndi amuna aja azi ndalama, chikondi chako unachiika pa ndalama, unatsutsa mau oti chikondi si ndalama,
[Chorus]
Ngakhale uti sorry ine sindinganveso,
Mwayi ndinakupasa, unaukana wekha,
Ngakhale uti Pepa, sindingakhululukeso, poti chikondi changa iwe unachikana,
[Verse 2]
Nditatopa ndikuyendela iwe ndinakusiya, ndinapeza mzako wina yemwe anandikonda, patangopita kanthawi ndinapeza chuma, pano wayamba kubwera kumandipepesa, wati ndikhuluruke ndikhuluruka Chani, poti zofuna zako iwe unazipeza,
[Chorus]
Ngakhale uti sorry, ine sindinganveso, Mwayi ndinakupasa unaukana wekha, ngakhale uti Pepa sindingakhululukeso, poti chikondi changa iwe unachikana
[Verse 3]
Ndithokoza namalenga poti wakumbuka, koma ndikungopepesa poti nthawi inatha, paja madzi akatayika samawolekaso, mwayi omwe unautaya azako anawutola akuwugwisa ntchito ndipo akunjoya, ngati ndikotheka mwina uzamupeza wina
[Outro]
George Chigomeee, mmmm this should be a lesson to all girls who they just love man because of money. Not real love. One day you will regret, thanks