[intro]
. Mmmm man ah moh
Moh
Mobisiyasi
[verse 1]
Tinkanyamuka ku ganyu mamawa
Olo kunja kuli mawawa
Kusunga ka fifty kupangira mawa
Pena kuseka inu penaso nkhawa
[Bridge]
Tikamaliza kumenya magobo,
Paphewa pako nditaponya nkono,
Uku tikuyankhulana pang'onopang'ono,
Tikadzaiphula tidzapita konko,
[chorus]
Tidzapita ku jamayika,
Pochokera ku Landani,
Akadzatifunsa wagwani,
Kaya tidzayankha kuti chani,
Tidzapita ku Jamayika,
Pochokera ku Landani,
Koma akadzatifunsa wagwani,
Kaya tidzayankha kuti chani,
[Verse 2]
Pa Chimwankhunda dam wakumbukira,
Unandipulumutsa ndikanamira,
Kukwera mapiri a aku sochi,
Moyo wathu nkayenda chonchi,
[Bridge]
Nde tikamaliza kusewera ndi dongo,
Pa phewa pako nditaponya mkono,
Uku tikuyankhulana pang'onopang'ono,
Tikadzaiphula tidzapita konko,
[Chorus)]
Tidzapita ku Jamayika,
Pochokera ku Landani,
Koma akadzatifunsa wagwani,
Kaya tidzayankha kuti chani,
Iweeee tidzapita ku Jamayika
Ife ku jamayikaaa
[outro]
Pano ndi pa foni kuyankhulana,
Uli kutali tinatayana,
Komabe maloto samang'amba,
Ndimakumbukira padzana