Artist: Newstar Malawi.
Song Title: Nkhani Yanga.
**Verse 1**
Nkhani yanga, kudzera mu nyimbo;
Nkhani yanga, ili mu nyimbo;
Nkhani yanga, imayenda mu nyimbo;
Nthawi zonse, ndidzamvera nyimbo;
**Chorus**
Ndikamakuona tsiku lilironse;
Mtima wanga umasowa ntendere;
Ndimafuna ntakuuza nkhani yanga;
Mtima wanga, ngodzara ndi nkhani;
Koma kuti kuuze, mawu akukanika;
Ndi chifukwa ndangoimba kanyimbo;
**Verse 2**
Pamene ndinali mu ululu;
Pamene zinthu zinali kundimvuta;
Munabwera m'moyo mwanga;
Munadza ngati kanyimbo kachikondi;
Ndinagwa nanu mu chikondi;
Osati kamba kamaonekedwe anu;
Chifukwa cha mtima wanu wachikondi;
Tiye tidzakhale limodzi mpaka muyaya;
**Chorus**
Ndikamakuona tsiku lilironse;
Mtima wanga umasowa ntendere;
Ndimafuna ntakuuza nkhani yanga;
Mtima wanga, ngodzara ndi nkhani;
Koma kuti kuuze, mawu akukanika;
Ndi chifukwa ndangoimba kanyimbo.
**Bridge**
Nkhani yanga, ikungoyenda mu mtima;
Nyimboyi ndi yako, awa ndi mawu anga;
Uzikumbukira, nthawi zonse, mpaka tidzakumananso;
Moyo wanga, wakhala wosavuta chifukwa cha iwe;
Ndimakukonda ngakhale uli kutali nane;
Uzikumbukira, nthawi zonse, tidzakumananso;
**Chorus**
Ndikamakuona tsiku lilironse,
Mtima wanga, umasowa ntendere;
Ndimafuna ntakuuza nkhani yanga;
Mtima wanga, ngodzara ndi nkhani;
Koma kuti kuuze, mawu akukanika;
Ndi chifukwa ndangoimba kanyimbo.