[Intro]
Kamwachoka son
Ehe ehe ehe ai
Filimoni ase
[Verse 1]
Ndiyambe ndimalonje
Eya Inu ndimalonje
Poti papita eh osaonana
Mawu mkumalankhulana
Inde koma osakumana
Uko kwathu uko
Uko kwakakhomwa
Anthu anga mulikuti
Ine mwana wanu
Inde wanu Filimoni
Azichemwari anga
Nanga Inu mulikuti
Azichimwene anga
Inuyo mulikuti kd
[Chorus]
Eh eh eh yeah
Filimoni abwera
Koma mwina silero
Mwinaso simawa
Koma ine ndibwera
Poti mmmh ndakusowani
[Verse 2]
Mwina mkumaganiza
Kuti chikondi chidatha
Poti nthawi ikutero
Ndiye ndayenera kutero
Kuti mwina tizakhale mfulu
Poti munthu amatopa
Akatopa amafuna potsamira
Lero mpomwe ndikukoza
Osatopa makolo
Inu abale anga nonse
Inde musatope
Nthawi ikubwera
Manja Anu azakondwa
Chorus
Eh akudalitseni Inu nose
Adani komaso abwenzi
Tonse ndife amodzi!
[Intro]
Kakhomwa Geto
Filimoni ase
Mwana wakumudzi
Eh eh eh ai
Kamwachoka son
I love You all