Artist: Newstar Malawi
Song Title: Ndakusowa
(Verse 1)
Ndakusowa monga momwe dzuwa limasowera nyenyezi usiku.
Ndiwe loto langa lomwe silidzafa.
Nthawi zonse, dzuwa likamalowa, ndimakumbukira nkhope yako.
Momwe inalili yowala, momwe tinkachezera bwino.
Tikakhala limodzi, kumanseka.
Ndimalimba mtima kuti one day tizachezanso.
(Chorus)
Tsiku likubwera lomwe lizachiritsa mabala athu.
Zipsera zamuntima mwathu zizachoka.
Tidzasiya kusowana, tizidzaonana every day.
Ndiwe munda wa muntima mwanga, ndiwe duwa limene silidzatha.
(Verse 2)
Ndidzapita nawe kulikonse,
monga tinkachitira poyamba.
Ndikamayenda munsewu,
umabwera muntima wanga.
Ndiwe moyo wanga, chikondi chako sichidzachoka muntima mwanga.
Ndimaganiza zaiwe nthawi zonse.
Ndimakumbukira zonse zomwe tinkachita.
(Chorus)
Tsiku likubwera lomwe lizachiritsa mabala athu.
Zipsera zamuntima mwathu zizachoka.
Tidzasiya kusowana, tizidzaonana every day.
Ndiwe munda wa muntima mwanga, ndiwe duwa limene silidzatha.
(Bridge)
Ndiwe chiyembekezo changa ndikamalira.
Ndiwe chizindikiro cha chikondi changa.
Ndiwe nyali kukagwa dima.
Ndiwe ambulera kukagwa mvura.
Ndiwe chofunda ndikazizidwa.
Ndimakukonda ngakhale muzowawa.
(Chorus)
Tsiku likubwera lomwe lizachiritsa mabala athu.
Zipsera zamuntima mwathu zizachoka.
Tidzasiya kusowana, tizidzaonana every day.
Ndiwe munda wa muntima mwanga, ndiwe duwa limene silidzatha.
(Outro)
Ndakusowa monga momwe dzuwa limasowera nyenyezi usiku.
Ndiwe loto langa lomwe silidzafa.
Nthawi zonse, dzuwa likamalowa, ndimakumbukira nkhope yako.
Momwe inalili yowala, momwe tinkachezera bwino.
Tikakhala limodzi, kumanseka.
Ndimalimba mtima kuti one day tizachezanso.
(I miss you, my lover you are my life. I'am your boy Yohane, Newstar Malawi)