(intro)
Eyoh Malawi!
Mfanawama rules
(acoustic vision)
(verse)
Kodi unayamba, wakhara!
iwe wakhara!
unayamba wakhara
kulingalila!?
Kodi unayamba wadekha!
iwe wadekha!
Kodi unayamba wadekha
kuziganizila!!
kuti akula bwanji mwana
opanda Bambo
kopanda mwambo
ooo!
kuti akula bwanji mwana osawona bambo
ooo!
(chorus)
Zisankho,! Zisankho, Zisankho
zamakolo
Zizuzinsa ana!
zisankho (x4)
(verse)
Khala pansi uzifunse
iwe uzifunse
kuti amati chani mwana
akawona amzake Iwo ali ndi Bambo
ndipo akukondedwa
Kodi amati chani mwana
iye amazifunsa
ine a daddy bwanji?
Kodi ananka kuti
nanga ndinalakwanji
kuti andisiye ndekha?!
ine ndekha?
iye amayang'anila kunjira
kuti Bambo atulukira
koma ayi sabwera!
(chorus)
Zisankho,! Zisankho, Zisankho
zamakolo
Zizuzinsa ana!
zisankho (x4)
(bridge)
Nkhawa zimayamba mwana
akamasilila
chikondi chabambo sachiziwa
amazati mwina anatisiya?
zikafika apa amalila!
chonde umuwuze!! ndilipo!!
ndilipo, wamoyo ndilipo!
koma Vuto zisankho zamakolo
makolo zimamuzunza mwana
(chorus)
Zisankho,! Zisankho, Zisankho
zamakolo
Zizuzinsa ana!
Zisankho (x4)
(outro)
unati tinasiyana
ndipo
tisamayenderane
poti uli ndi chibwezi
ndiye tisamayimbilane ma phone
koma mkamayimba ndimafuna ndimveko mawu amwana
ndicheze naye
aziwe ndilipo wamoyo ndilipo
(outro)
Home sounds production